[1] Mwana wanga, mvera mawu anga; usunge bwino malamulo angawa.
[2] Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
[3] Uchite ngati wawamangirira pa zala zako, ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
[4] Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
[5] Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
[6] Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga ndinasuzumira pa zenera.
[7] Ndinaona pakati pa anthu opusa, pakati pa anyamata, mnyamata wina wopanda nzeru.
[8] Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
[9] Inali nthawi yachisisira madzulo, nthawi ya usiku, kuli mdima.
[10] Ndipo mkaziyo anadzakumana naye, atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
[11] (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve, iye ndi wosakhazikika pa khomo.
[12] Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika, ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
[13] Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
[14] “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano. Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
[15] Choncho ndinabwera kudzakumana nawe; ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
[16] Pa bedi panga ndayalapo nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
[17] Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
[18] Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa; tiye tisangalatsane mwachikondi!
[19] Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako; wapita ulendo wautali:
[20] Anatenga thumba la ndalama ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
[21] Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo; amukopa ndi mawu ake oshashalika.
[22] Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo ngati ngʼombe yopita kukaphedwa, monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
[23] mpaka muvi utalasa chiwindi chake, chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe, osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
[24] Tsono ana inu, ndimvereni; mvetsetsani zimene ndikunena.
[25] Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu; musasochere potsata njira zake.
[26] Paja iye anagwetsa anthu ambiri; wapha gulu lalikulu la anthu.
[27] Nyumba yake ndi njira yopita ku manda, yotsikira ku malo a anthu akufa.