[6] Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti: Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?