[12] Popeza kuti dookolo silinali labwino kukhalako nthawi yozizira anthu ambiri anaganiza kuti tichoke. Ife tinkayembekeza kukafika ku Foinikisi ndi kukhala kumeneko nthawi yachisanu. Ili linali dooko la ku Krete, limene limaloza kummwera cha kumadzulo ndiponso kumpoto cha kumadzulo.