[24] Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge.” Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati, “Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo ndi kuchita maere pa zovala zangazo.” Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.