[1] Pamene ndichiritsa Israeli, machimo a Efereimu amaonekera poyera ndiponso milandu ya Samariya sibisika. Iwo amachita zachinyengo, mbala zimathyola nyumba, achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
[2] Koma sazindikira kuti Ine ndimakumbukira zoyipa zawo zonse. Azunguliridwa ndi zolakwa zawo; ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.
[3] “Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo, akalonga amasekerera mabodza awo.
[4] Onsewa ndi anthu azigololo, otentha ngati moto wa mu uvuni, umene wophika buledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
[5] Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu akalonga amaledzera ndi vinyo, ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
[6] Mitima yawo ili ngati uvuni; amayandikira Mulungu mwachiwembu. Ukali wawo umanyeka usiku wonse, mmawa umayaka ngati malawi a moto.
[7] Onsewa ndi otentha ngati uvuni, amapha olamulira awo. Mafumu awo onse amagwa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.
[8] “Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena; Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
[9] Alendo atha mphamvu zake, koma iye sakuzindikira. Tsitsi lake layamba imvi koma iye sakudziwa.
[10] Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa, koma pa zonsezi iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake kapena kumufunafuna.
[11] “Efereimu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru. Amayitana Igupto namapita ku Asiriya.
[12] Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga; ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga. Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi ndidzawakola.
[13] Tsoka kwa iwo, chifukwa andisiya Ine! Chiwonongeko kwa iwo, chifukwa andiwukira! Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa koma amayankhula za Ine monama.
[14] Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima, koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo. Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano, koma amandifulatira.
[15] Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa, koma amandikonzera chiwembu.
[16] Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba; ali ngati uta woonongeka. Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mawu awo achipongwe. Motero iwo adzasekedwa mʼdziko la Igupto.