[20] Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.